Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 94:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pamene ndinati, Litereka phazi langa,Cifundo canu, Mulungu, cinandicirikiza.

19. Pondicurukira zolingalira zanga m'kati mwanga,Zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.

20. Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wacifumu wa kusakaza,Wakupanga cobvuta cikhale lamulo?

21. Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama,Namtsutsa wa mwazi wosacimwa.

22. Koma Yehova wakhala msanje wanga;Ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

23. Ndipo anawabwezera zopanda pace zao,Nadzawaononga m'coipa cao;Yehova Mulungu wathu adzawaononga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 94