1. Mulungu wakubwezera cilango,Yehova, Mulungu wakubwezera cilango, muoneke wowala.
2. Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi:Bwezerani odzikuza coyenera iwo.
3. Oipa adzatumpha ndi cimwemwe kufikira liti, Yehova?Oipa adzatero kufikira liti?
4. Anena mau, alankhula zawawa;Adzitamandira onse ocita zopanda pace.
5. Aphwanya anthu anu, Yehova,Nazunza colandira canu.
6. Amapha wamasiye ndi mlendo,Nawapha ana amasiye.