Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 92:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba ku nthawi yonse.

9. Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,Pakuti, taonani, adani anu adzatayika;Ocita zopanda pace onse adzamwazika.

10. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;Anandidzoza mafuta atsopano.

11. Diso langa lapenya cokhumba ine pa iwo ondilalira,M'makutu mwanga ndamva cokhumba ine pa iwo akucita zoipa akundiukira.

12. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;Adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano.

13. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova,Adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.

14. Atakalamba adzapatsanso zipatso;Adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri:

15. Kulalikira kuti Yehova ngwolunjika;Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe cosalungama.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 92