Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 92:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nkokoma kuyamika Yehova,Ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu:

2. Kuonetsera cifundo canu mamawa,Ndi cikhulupiriko canu usiku uli wonse.

3. Pa coyimbira ca zingwe khumi ndi pacisakasa;Pazeze ndi kulira kwace.

4. Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kucita kwanu,Ndidzapfuula mokondwera pa nchito ya manja anu.

5. Ha! nchito zanu nzazikuru, Yehova,Zolingalira zanu nzozama ndithu.

6. Munthu wopulukira sacidziwa;Ndi munthu wopusa sacizindikira ici;

7. Cakuti pophuka oipa ngati msipu,Ndi popindula ocita zopanda pace;Citero kuti adzaonongeke kosatha:

8. Koma Inu, Yehova, muli m'mwamba ku nthawi yonse.

9. Pakuti, taonani, adani anu, Yehova,Pakuti, taonani, adani anu adzatayika;Ocita zopanda pace onse adzamwazika.

10. Koma munakweza nyanga yanga ngati ya njati;Anandidzoza mafuta atsopano.

11. Diso langa lapenya cokhumba ine pa iwo ondilalira,M'makutu mwanga ndamva cokhumba ine pa iwo akucita zoipa akundiukira.

12. Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa;Adzakula ngati mkungudza wa ku Lebano.

13. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova,Adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 92