Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 9:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi.Msanje m'nyengo za nsautso;

10. Ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu;Pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

11. Yimbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni;Lalikirani mwa anthu nchito zace.

12. Pakuti Iye wofuna camwazi awakumbukila;Saiwala kulira kwa ozunzika.

13. Ndicitireni cifundo, Yehova;Penyani kuzunzika kwanga kumene andicitira ondidawo,Inu wondinyamula kundicotsa ku zipata za imfa;

14. Kuti ndibukitse lemekezo lanu lonse;Pa bwalo la mwana wamkazi wa Ziyoni,Ndidzakondwera naco cipulumutso canu.

15. Amitundu anagwa m'mbuna imene anaikumba:Lakodwa phazi lao muukonde anaucha.

16. Anadziwika Yehova, anacita kuweruza:Woipayo anakodwa ndi nchito ya manja ace.

17. Oipawo adzabwerera kumanda,Inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

18. Pakuti sadzaiwalika nthawi zonse waumphawi,Kapena ciyembekezo ca ozunzika sicidzaonongeka kosatha.

19. Ukani, Yehova, asalimbike munthu;Amitundu aweruzidwe pankhope panu.

20. Muwacititse mantha, Yehova; Adziwe amitundu kuti ali anthu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 9