Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 9:11-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Yimbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni;Lalikirani mwa anthu nchito zace.

12. Pakuti Iye wofuna camwazi awakumbukila;Saiwala kulira kwa ozunzika.

13. Ndicitireni cifundo, Yehova;Penyani kuzunzika kwanga kumene andicitira ondidawo,Inu wondinyamula kundicotsa ku zipata za imfa;

Werengani mutu wathunthu Masalmo 9