1. Ndidzayamika Yehova ndi mtima wanga wonse;Ndidzawerengera zodabwiza zanu zonse.
2. Ndidzakondwerera ndi kusekera mwa Inu;Ndidzayimbira dzina lanu, Wam'mwambamwamba Inu.
3. Pobwerera m'mbuyo adani anga,Akhumudwa naonongeka pankhope panu,
4. Pakuti mwandiweruzira mlandu wanga;Mwakhala pa mpando wacifumu, Woweruza wolungama.
5. Mwadzudzula amitundu, mwaononga woipayo,Mwafafaniza dzina lao ku nthawi Yomka muyaya.
6. Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse;Ndipo midziyo mwaipasula,Cikumbukilo cao pamodzi catha.