Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 88:5-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Wotayika pakati pa akufa,Ngati ophedwa akugona m'manda,Amene simuwakumbukilanso;Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

6. Munandiika kunsi kwa dzenje,Kuti mdima, kozama.

7. Mkwiyo wanu utsamira pa ine,Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.

8. Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;Munandiika ndiwakhalire conyansa:Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine.

9. Diso langa lapuwala cifukwa ca kuzunzika kwanga:Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse;Nditambalitsira manja anga kwa Inu.

10. Kodi mudzacitira akufa zodabwiza?Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani?

11. Adzafotokozera cifundo canu kumanda kodi,Cikhulupiriko canu ku malo a cionongeko?

12. Zodabwiza zanu zidzadziwika mumdima kodi,Ndi cilungamo canu m'dziko la ciiwaliko?

13. Koma ndinapfuulira kwa Inu, Yehova,Ndipo pemphero langa likumika Inu mamawa.

14. Yehova mutayiranji moyo wanga?Ndi kundibisira nkhope yanu?

15. Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;Posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.

16. Kuzaza kwanu kwandimiza;Zoopsa zanu zinandiononga,

17. Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;Zinandizinga pamodzi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 88