Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 88:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Koma ndinapfuulira kwa Inu, Yehova,Ndipo pemphero langa likumika Inu mamawa.

14. Yehova mutayiranji moyo wanga?Ndi kundibisira nkhope yanu?

15. Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga;Posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru.

16. Kuzaza kwanu kwandimiza;Zoopsa zanu zinandiononga,

17. Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse;Zinandizinga pamodzi.

18. Munandicotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa,Odziwana nane akhala kumdima.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 88