Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 88:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, Mulungu wa cipulumutso canga,Ndinapfuula pamaso panu usana ndi usiku,

2. Pemphero langa lidze pamaso panu;Mundicherere khutu kukuwa kwanga:

3. Pakuti mzimu wanga wadzala nao mabvuto,Ndi moyo wanga wayandikira kumanda.

4. Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje;Ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu:

5. Wotayika pakati pa akufa,Ngati ophedwa akugona m'manda,Amene simuwakumbukilanso;Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu.

6. Munandiika kunsi kwa dzenje,Kuti mdima, kozama.

7. Mkwiyo wanu utsamira pa ine,Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse.

8. Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali;Munandiika ndiwakhalire conyansa:Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 88