9. Indedi cipulumutso cace ciri pafupi ndi iwo akumuopa Iye;Kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.
10. Cifundo ndi coonadi zakomanizana;Cilungamo ndi mtendere zapsompsonana,
11. Coonadi ciphukira m'dziko;Ndi cilungamo casuzumira ciri m'mwamba.
12. Inde Yehova adzapereka zokoma;Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zace.
13. Cilungamo cidzamtsogolera; Nicidzamkonzera mapazi ace njira.