Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 85:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Munacotsa mphulupulu ya anthu anu,Munafotsera zolakwa zao zonse.

3. Munabweza kuzaza kwanu konse;Munabwerera ku mkwiyo wanu wotentha.

4. Mutibweze, Mulungu wa cipulumutso cathu,Nimuletse udani wanu wa pa ife.

5. Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse?Kodi mudzakhala cikwiyire mibadwo mibadwo?

6. Kodi simudzatipatsanso moyo,Kuti anthu anu akondwerere ndi Inu?

7. Tionetseni cifundo canu, Yehova,Tipatseni cipulumutso canu.

8. Ndidzamva colankhula Mulungu Yehova;Pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ace, ndi okondedwa ace;Koma asabwererenso kucita zapusa.

9. Indedi cipulumutso cace ciri pafupi ndi iwo akumuopa Iye;Kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.

10. Cifundo ndi coonadi zakomanizana;Cilungamo ndi mtendere zapsompsonana,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 85