Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 8:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Yehova, Ambuye wathu,Dzina lanu liposadi nanga pa dziko lonse lapansi!Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.

2. M'kamwa mwa makanda ndi oyamwamunakhazikitsamphamvu,Cifukwa ca otsutsana ndi Inu,Kuti muwaletse mdani ndi wobwezera cilango.

3. Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, nchito ya zala zanu,Mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,

4. Munthu ndani kuti mumkumbukila?Ndi mwana wa munthu kuti muceza naye?

5. Pakuti munamcepsa pang'ono ndi Mulungu,Munambveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 8