1. Mulungu adziwika mwa Yuda:Dzina lace limveka mwa Israyeli.
2. Msasa wace unali m'Salemu, Ndipo pokhala Iye m'Ziyoni.
3. Pomwepo anatyola mibvi ya paota;Cikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4. Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli acifwamba.
5. Olimba mtima cifunkhidwa cuma cao, agona tulo tao;Amuna onse amphamvu asowa manja ao.
6. Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,Gareta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.