Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 71:10-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakuti adani anga alankhula za ine;Ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,

11. Ndi kuti, Wamsiya Mulungu:Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa,

12. Musandikhalire kutali, Mulungu;Fulumirani kundithandiza, Mulungu;

13. Adani a moyo wanga acite manyazi, nathawe;Cotonza ndi cimpepulo zikute ondifunira coipa,

14. Koma ine ndidzayembekeza kosaleka,Ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani.

15. Pakamwa panga padzafotokozera cilungamo canu,Ndi cipulumutso canu tsiku lonse;Pakuti sindidziwa mawerengedwe ace.

16. Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova;Ndidzachula cilungamo canu, inde canu cokha.

17. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga;Ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.

18. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu;Kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu,Mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.

19. Cilungamo canunso, Mulungu, cifikira kuthambo;Inu amene munacita zazikuru,Akunga Inu ndani, Mulungu?

20. Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa,Mudzatipatsanso moyo,Ndi kutitenganso munsi mwa dziko.

21. Mundionjezere ukulu wanga,Ndipo munditembenukire kundisangalatsa,

22. Ndiponso ndidzakuyamikani ndi cisakasa,Kubukitsa coonadi canu, Mulungu wanga;Ndidzakuyimbirani Nyimbo ndi zeze,Ndinu Woyerayo wa Israyeli.

23. Milomo yanga idzapfuula mokondwera poyimbira Inu Nyimbo;Inde, moyo wanga umene munaombola.

24. Lilime langa lomwe lidzalankhula za cilungamo canu tsiku lonse:Pakuti ofuna kundicitira coipa acita manyazi, nadodoma.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 71