3. Koma olungama akondwere; atumphe ndi cimwemwe pamaso pa Mulungu;Ndipo asekere naco cikondwerero.
4. Yimbirani Yehova, liyimbireni Nyimbo dzina lace;Undirani mseu Iye woberekekayo kucidikha;Dzina lace ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi cimwemwe pamaso pace.
5. Mulungu, mokhala mwace mayera,Ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.
6. Mulungu amangitsira banjaanthu a pa okha;Aturutsa am'ndende alemerere;Koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.
7. Pakuturuka paja, Inu Mulungu, ndi kutsogolera anthu anu,Pakuyenda paja Inu m'cipululu;
8. Dziko lapansi linagwedezeka,Inde thambo linakhapamaso pa Mulungu;Sinai lomwe linagwedezeka pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israyeli.
9. Inu, Mulungu, munabvumbitsa cimvula,Munatsitsimutsa colowa canu pamene cidathodwa.
10. Gulu lanu linakhala m'dziko muja:Mwa ukoma wanu munalikonzera ozunzika, Mulungu.