Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 68:19-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Wolemekezeka Ambuye, tsiku ndi tsiku atisenzera katundu,Ndiye Mulungu wa cipulumutso cathu.

20. Mulungu akhala kwa ife Mulungu wa cipulumutso;Ndipo Yehova Ambuye ali nazo zopulumutsira kuimfa.

21. Indedi Mulungu adzaphwanya mutu wa adani ace,Pakati pa mutu pa iye woyendabe m'kutsutsika kwace.

22. Ambuye anati, Ndidzawatenganso ku Basana,Ndidzawatenganso kozama kwa nyanja:

23. Kuti ubviike phazi lako m'mwazi,Kuti malilime a agaru ako alaweko adani ako.

24. Anapenya mayendedwe anu, Mulungu,Mayendedwe a Mulungu wanga, Mfumu yanga, m'malo oyera.

25. Oyimbira anatsogolera, oyimba zoyimba anatsata m'mbuyo,Pakatipo anamwali oyimba mangaka.

26. Lemekezani Mulungu m'masonkhano,Ndiye Ambuye, inu a gwero la Israyeli.

27. Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwacita ufumu,Akuru a Yuda, ndi a upo wao,Akulu a Zebuloni, akulu a Naftali.

28. Mulungu wako analamulira mphamvu yako:Limbitsani, Mulungu, cimene munaticitira.

29. Cifukwa ca Kacisi wanu wa m'YerusalemuMafumu adzabwera naco caufulu kukupatsani.

30. Dzudzulani cirombo ca m'bango,Khamu la mphongo ndi zipfulula za anthu,Yense wakudzigonjera ndi ndarama zasiliva;Anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.

31. Akulu adzafumira ku Aigupto;Kushi adzafulumira kutambalitsa manja ace kwa Mulungu.

32. Yimbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;Yimbirani Ambuye zomlemekeza;

33. Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba, oyambira kale lomwe;Taonani; amveketsa liu lace, ndilo liu lamphamvu.

34. Bvomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;Ukulu wace uli pa Israyeli,Ndi mphamvu yace m'mitambo.

35. Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu;Mulungu wa Israyeli ndiye amene apatsa anthu ace mphamvu ndi cilimbiko.Alemekezeke Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 68