1. Auke Mulungu, abalalike adani ace;Iwonso akumuda athawe pamaso pace.
2. Muwacotse monga utsi ucotseka; Monga phula lisungunuka pamoto,Aonongeke oipa pamaso pa Mulungu.
3. Koma olungama akondwere; atumphe ndi cimwemwe pamaso pa Mulungu;Ndipo asekere naco cikondwerero.
4. Yimbirani Yehova, liyimbireni Nyimbo dzina lace;Undirani mseu Iye woberekekayo kucidikha;Dzina lace ndiye Yehova; ndipo tumphani ndi cimwemwe pamaso pace.
5. Mulungu, mokhala mwace mayera,Ndiye Atate wa ana amasiye, ndi woweruza wa akazi amasiye.
6. Mulungu amangitsira banjaanthu a pa okha;Aturutsa am'ndende alemerere;Koma opikisana naye akhala m'dziko lopanda madzi.