Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 66:4-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,Ndipo lidzakuyimbirani;Adzayimbira dzina lanu.

5. Idzani, muone nchito za Mulungu;Zocitira Iye ana a anthu nzoopsa.

6. Anasanduliza nyanja ikhale mtunda:Anaoloka mtsinje coponda pansi:Apo tinakondwera mwa Iye.

7. Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha;Maso ace ayang'anira amitundu;Opikisana ndi Iye asadzikuze.

8. Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace:

9. Iye amene asunga moyo wathu tingafe,Osalola phazi lathu literereke.

10. Pakati munatiyesera, Mulungu:Munatiyenga monga ayenga siliya.

11. Munapita nafe kuukonde;Munatisenza cothodwetsa pamsana pathu.

12. Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu;Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa.

13. Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza,Ndidzakucitirani zowinda zanga,

14. Zimene inazichula milomo yanga,Ndinazinena pakamwa panga pasautsika ine.

15. Ndidzakufukizirani nsembe zapsereza zonona,Pamodzi ndi cofukiza ca mphongo za nkhosa;Ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.

16. Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu,Ndipo ndidzafotokozera zonse anazicitira moyo wanga,

17. Ndinampfuulira Iye pakamwa panga,Ndipo ndinamkuza ndi lilime langa,

18. Ndikadasekera zopanda pace m'mtima mwanga,Ambuye sakadamvera:

19. Koma Mulungu anamvadi; Anamvera mau a pemphero langa,

20. Wolemekezeka Mulungu,Amene sanandipatutsira ine pemphero langa, kapena cifundo cace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 66