Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 66:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pfuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi.

2. Yimbirani ulemerero wa dzina lace;Pomlemekeza mumcitire ulemerero.

3. Nenani kwa Mulungu, Ha, nchito zanu nzoopsa nanga!Cifukwa ca mphamvu yanu yaikuru adani anu adzagonjera Inu,

4. Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani,Ndipo lidzakuyimbirani;Adzayimbira dzina lanu.

5. Idzani, muone nchito za Mulungu;Zocitira Iye ana a anthu nzoopsa.

6. Anasanduliza nyanja ikhale mtunda:Anaoloka mtsinje coponda pansi:Apo tinakondwera mwa Iye.

7. Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha;Maso ace ayang'anira amitundu;Opikisana ndi Iye asadzikuze.

8. Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu,Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace:

9. Iye amene asunga moyo wathu tingafe,Osalola phazi lathu literereke.

10. Pakati munatiyesera, Mulungu:Munatiyenga monga ayenga siliya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 66