Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 55:14-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Tinapangirana upo wokoma,Tinaperekeza khamu la anthu popita ku nyumba ya Mulungu.

15. Imfa iwagwere modzidzimutsa,Atsikire kumanda ali amoyo:Pakuti m'mokhala mwao muli zoipa pakati pao,

16. Koma ine ndidzapfuulira kwa Mulungu;Ndipo Yehova atizandipulumutsa.

17. Madzulo, m'mawa, ndi msana ndidzadandaula, ndi kubuula,Ndipo adzamva mau anga.

18. Anaombola moyo wanga ku nkhondo yondilaka, ndikhale mumtendere:Pakuti ndiwo ambiri okangana nane.

19. Mulungu adzamva, nadzawasautsa,Ndiye wokhalabe ciyambire kale lomwe.Popeza iwowa sasinthika konse,Ndipo saopa Mulungu.

20. Anaturutsa manja ace awagwire iwo akuyanjana naye:Anaipsa pangano lace.

21. Pakamwa pace mposalala ngati mafuta amkaka,Koma mumtima mwace munali nkhondo:Mau ace ngofewa ngati mafuta oyenga,Koma anali malupanga osololasolola.

22. Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iyeadzakugwiriziza:Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

23. Koma Inu, Mulungu, mudzawatsitsira ku dzenje la cionongeko:Anthu okhetsa mwazi ndi acinyengo masiku ao sadzafikira nusu;Koma ine ndidzakhulupirira Inu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 55