Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 54:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.

2. Imvani pemphero langa, Mulungu;Cherani khutu mau a pakamwa panga.

3. Pakuti alendo andiukira,Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;Sadziikira Mulungu pamaso pao.

4. Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga:Ambuye ndiye wacirikiza moyo wanga.

5. Adzabwezera coipa adani anga:Aduleni m'coonadi canu.

6. Ine mwini ndidzapereka nsembe kwa Inu:Ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 54