1. Citsiru cimati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.Acita zobvunda, acita cosalungama conyansa;Kulibe wakucita bwino.
2. Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu,Kuti aone ngati aliko wanzeru, Wakufuna Mulungu.
3. Onse anabwerera; anabvunda mtima pamodzi;Palibe mmodzi wakucita bwino, nnena mmodzi.