10. Mundilengere mtima woyera, Mulungu;Mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.
11. Musanditaye kundicotsa pamaso panu;Musandicotsere Mzimu wanu Woyera.
12. Mundibwezere cimwemwe ca cipulumutso canu;Ndipo mzimu wakulola undigwirizize.
13. Pomwepo ndidzalangiza ocimwa njira zanu;Ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.
14. Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu,Ndinu Mulungu wa cipulumutso canga;Lilime langalidzakweza Nyimbo ya cilungamo canu.
15. Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;Ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.
16. Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;Nsembe yopsereza simuikonda.
17. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.
18. Citirani Ziyoni cokoma monga mwa kukondwera kwanu;Mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
19. Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zacilungamo,Ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu:Pamenepo adzaperekaNg'ombe pa guwa lanu la nsembe.