Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 50:5-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Mundisonkhanitsire okondedwa anga;Amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

6. Ndipo zakumwamba zionetsera cilungamo cace;Pakuti Mulungu mwini wace ndiye woweruza.

7. Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena;Israyeli, ndipo ndidzacita mboni pa iwe:Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.

8. Sindikudzudzula iwe cifukwa ca nsembe zako;Popeza nsembe zako zopsereza ziri pamaso panga cikhalire.

9. Sindidzatenga ng'ombe m'nyumbamwako,Kapena mbuzi m'makola mwako.

10. Pakuti zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga,Ndi ng'ombe za pa mapiri zikwi.

11. Ndidziwa mbalame zonse za m'mapiri:Ndipo nyama za kuthengo ziri ndi Ine.

12. Ndikamva njala, sindidzakuuza:Pakuti dziko lonse ndi langa, ndi kudzala kwace komwe.

13. Kodi ndidzadya nyama ya ng'ombe,Kapena kumwa mwazi wa mbuzi?

14. Pereka kwa Mulungu nsembe yaciyamiko;Numcitire Wam'mwambamwamba cowinda cako:

15. Ndipo undiitane tsiku la cisautso:Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.

16. Koma kwa woipa Mulungu anena,Uli nao ciani malemba anga kulalikira,Ndi kuchula pangano langa pakamwa pako?

17. Popeza udana naco cilangizo,Nufulatira mau anga.

18. Pakuona mbala, ubvomerezana nayo,Nucita nao acigololo.

19. Pakamwa pako mpocita zocimwa,Ndipo lilime lako likonza cinyengo.

20. Ukhala, nuneneza mbale wako;Usinjirira mwana wa mai wako.

21. Izi unazicita iwe, ndipo ndinakhala cete Ine;Unayesa kuti ndifanana nawe:Ndidzakudzudzula, ndi kucilongosola pamaso pako.

22. Dziwitsani ici inu oiwala Mulungu,Kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi:

23. Wopereka nsembe yaciyamiko andilemekeza Ine;Ndipo kwa iye wosunga mayendedwe aceNdidzamuonetsa cipulumutso ca Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 50