18. Pakuona mbala, ubvomerezana nayo,Nucita nao acigololo.
19. Pakamwa pako mpocita zocimwa,Ndipo lilime lako likonza cinyengo.
20. Ukhala, nuneneza mbale wako;Usinjirira mwana wa mai wako.
21. Izi unazicita iwe, ndipo ndinakhala cete Ine;Unayesa kuti ndifanana nawe:Ndidzakudzudzula, ndi kucilongosola pamaso pako.
22. Dziwitsani ici inu oiwala Mulungu,Kuti ndingakumwetuleni, ndipo mungasowepo mpulumutsi:
23. Wopereka nsembe yaciyamiko andilemekeza Ine;Ndipo kwa iye wosunga mayendedwe aceNdidzamuonetsa cipulumutso ca Mulungu.