Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 50:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu wa milungu, Yehova, wanena,Aitana dziko lapansi kuyambira kuturuka kwa dzuwa kufikira kulowa kwace.

2. Mulungu awalira m'Ziyoni, mokongola mwangwiro.

3. Adzafika Mulungu wathu, ndipo sadzakhala cete:Moto udzanyeka pankhope pace,Ndipo pozungulira pace padzasokosera kwakukuru.

4. Kumwamba adzaitana zakumwamba,Ndi dziko lapansi, kuti aweruze anthu ace:

5. Mundisonkhanitsire okondedwa anga;Amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

6. Ndipo zakumwamba zionetsera cilungamo cace;Pakuti Mulungu mwini wace ndiye woweruza.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 50