Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 49:9-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kuti akhale ndi moyo osafa,Osaona cibvundi.

10. Pakuti aona anzeru amafa,Monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,Nasiyira ena cuma cao.

11. Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala cikhalire,Ndi mokhala iwo ku mibadwo mibadwo;Achapo dzina lao padziko pao.

12. Koma munthu wa ulemu wace sakhalitsa:Afanana ndi nyama za kuthengo, afanana nazo.

13. Njira yao yino ndiyo kupusa kwao:Koma akudza m'mbuyo abvomereza mau ao.

14. Aikidwa m'manda ngati nkhosa;Mbusa wao ndi imfa:Ndipo m'mawa mwace oongoka mtima adzakhala mafumu ao;Ndipo maonekedwe ao adzanyekera kumanda, kuti pokhala pace padzasowa.

15. Koma Mulungu adzaombola moyo wanga ku mphamvu ya manda:Pakuti adzandilandira ine.

16. Usaope polemezedwa munthu,Pocuruka ulemu wa nyumba yace;

17. Pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kali konse;Ulemu wace sutsika naye kumtsata m'mbuyo.

18. Angakhale anadalitsa moyo wace pokhala ndi moyo,Ndipo anthu akulemekeza iwe, podzicitira wekha zokoma,

19. Adzamuka ku mbadwo wa makolo ace;Sadzaona kuunika nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 49