Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 49:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Dzamveni kuno, anthu inu nonse;Cherani khutu, inu nonse amakono,

2. Awamba ndi omveka omwe,Acuma ndi aumphawi omwe.

3. Pakamwa panga padzanena zanzeru;Ndipo cilingiriro ca mtima wanga cidzakhala ca cidziwitso.

4. Ndidzachera khutu kufanizo:Ndidzafotokozera cophiphiritsa canga poyimbira.

5. Ndidzaoperanji masiku oipa,Pondizinga amphulupulu onditsata kucidendene?

6. Iwo akutama kulemera kwao;Nadzitamandira pa kucuruka kwa cuma cao;

7. Kuombola mbale sangadzamuombole,Kapena kumperekera dipo kwa Mulungu:

8. (Popeza ciombolo ca moyo wao nca mtengo wace wapatali,Ndipo cilekeke nthawi zonse)

9. Kuti akhale ndi moyo osafa,Osaona cibvundi.

10. Pakuti aona anzeru amafa,Monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo,Nasiyira ena cuma cao.

11. Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala cikhalire,Ndi mokhala iwo ku mibadwo mibadwo;Achapo dzina lao padziko pao.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 49