Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 46:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,Thandizo lopezekeratu m'masautso.

2. Cifukwa cace sitidzacita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi,Angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja;

3. Cinkana madzi ace akokoma, nacita thobvu,Nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwace.

4. Pali mtsinje, ngalande zace zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba,

5. Mulungu ali m'kati mwace, sudzasunthika:Mulungu adzauthandiza mbanda kuca.

6. Amitundu anapokosera; maufumu anagwedezeka:Ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.

7. Yehova wa makamu ali ndi ife;Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 46