Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 42:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje;Motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.

2. Moyo wanga uli ndi ludzu la kwa Mulungu, la kwa Mulungu wamoyo:Ndikadze liti kuoneka pamaso pa Mulungu?

3. Misozi yanga yakhalangati cakudya canga,Usana ndi usiku;Pakunena iwo kwa ine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?

4. Ndizikumbukila izi ndipo nditsanulira moyo wanga m'kati mwa ine,Pakuti ndidafopita ndi unyinji wa anthu,Ndinawatsogolera ku nyumba ya Mulungu, ndi mau akuyimbitsa ndi kuyamika,Ndi unyinji wakusunga dzuwa lokondwera.

5. Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikansoCifukwa ca cipulumutso ca nkhope yace.

6. Mulungu wanga, moyo wangaUdziweramira m'kati mwanga;Cifukwa cace ndikumbukila Inu m'dziko la Yordano,Ndi mu Ahermone, m'kaphiri ka Mizara.

7. Madzi akuya aitanizana ndi madzi akuya,Pa mkokomo wa matiti anu: Mafunde onse a nyondonyondo anandimiza ine.

8. Koma usana Yehova adzalamulira cifundo cace,Ndipo usiku Nyimbo yace idzakhala ndi ine.Inde pemphero la kwa Yehova wa moyowanga.

9. Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala cifukwa ninji?Ndimayenderanji wakulira Cifukwa ca kundipsinja mdaniyo?

10. Adani anga andinyoza ndi kundityola mafupa anga;Pakunena ndine dzuwa lonse,Mulungu wako ali kuti?

11. Udziweramiranji moyo wanga iwe?Ndi kuzingwa m'kati mwanga?Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso,Ndiye cipulumutso ca nkhope yanga ndi Mulungu wanga,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 42