Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 41:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;Mumtima mwace adzisonkhera zopanda pace:Akamka nayenda namakanena:

7. Onse akudana nane andinong'onezerana;Apangana condiipsa ine.

8. Camgwera cinthu coopsa, ati;Popeza ali gonire sadzaukanso.

9. Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga,Anandikwezera cidendene cace.

10. Koma Inu, Yehova, mundicitire cifundo, ndipo mundiutse,Kuti ndiwabwezere.

11. Umo ndidziwa kuti mukondwera ndi ine,Popeza mdani wanga sandiseka.

12. Ndipo ine, mundigwirizize m'ungwiro wanga,Ndipo mundiike pankhope panu ku nthawi yamuyaya.

13. Wodalitsika Yehova, Mulungu wa Israyeli,Kucokera nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha.Amen, ndi Amen.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 41