3. Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;Podwala iye mukonza pogona pace,
4. Ndinati ine, Mundicitire cifundo, Yehova:Ciritsani mtima wanga; pakuti ndacimwira Inu.
5. Adani anga andinenera coipa, ndi kuti,Adzafa liti, ndi kutayika dzina lace?
6. Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;Mumtima mwace adzisonkhera zopanda pace:Akamka nayenda namakanena:
7. Onse akudana nane andinong'onezerana;Apangana condiipsa ine.
8. Camgwera cinthu coopsa, ati;Popeza ali gonire sadzaukanso.
9. Ngakhale bwenzi langa leni leni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga,Anandikwezera cidendene cace.
10. Koma Inu, Yehova, mundicitire cifundo, ndipo mundiutse,Kuti ndiwabwezere.