Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 41:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wodala iye amene asamalira wosauka:Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa:

2. Yehova adzamsunga, nadzamsunga ndi moyo, ndipo adzadalitsika pa dziko lapansi;Ndipo musampereke ku cifuniro ca adani ace.

3. Yehova adzamgwiriziza pa kama wodwalira;Podwala iye mukonza pogona pace,

4. Ndinati ine, Mundicitire cifundo, Yehova:Ciritsani mtima wanga; pakuti ndacimwira Inu.

5. Adani anga andinenera coipa, ndi kuti,Adzafa liti, ndi kutayika dzina lace?

6. Ndipo akadza kundiona wina angonena bodza;Mumtima mwace adzisonkhera zopanda pace:Akamka nayenda namakanena:

7. Onse akudana nane andinong'onezerana;Apangana condiipsa ine.

8. Camgwera cinthu coopsa, ati;Popeza ali gonire sadzaukanso.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 41