Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 38:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti mibvi yanu yandilowa,Ndi dzanja lanu landigwera.

3. Mumnofu mwanga mulibe camoyo cifukwa ca ukali wanu;Ndipo m'mafupa anga simuzizira, cifukwa ca colakwa canga.

4. Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga:Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.

5. Mabala anga anunkha, adaola, Cifukwa ca kupusa kwanga.

6. Ndapindika, ndawerama kwakukuru;Ndimayenda woliralira tsiku lonse.

7. Pakuti m'cuuno mwanga mutentha kwambiri;Palibe pamoyo m'mnofu mwanga,

8. Ndafoka ine, ndipo ndacinjizidwa:Ndabangula cifukwa ca kumyuka mtima wanga.

9. Ambuye, cikhumbo canga conse ciri pamaso panu;Ndipo kubuula kwanga sikubisika kwa Inu.

10. Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yacoka:Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandicokera.

11. Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;Ndipo anansi anga aima patali.

12. Ndipo andichera misampha iwo akufuna moyo wanga;Ndipo iwo akuyesa kundicitira coipa alankhula zoononga,Nalingirira zonyenga tsiku lonse.

13. Koma ine, monga gonthi, sindimva;Ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga.

14. Inde ndikunga munthu wosamva,Ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 38