Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 38:10-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yacoka:Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandicokera.

11. Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga;Ndipo anansi anga aima patali.

12. Ndipo andichera misampha iwo akufuna moyo wanga;Ndipo iwo akuyesa kundicitira coipa alankhula zoononga,Nalingirira zonyenga tsiku lonse.

13. Koma ine, monga gonthi, sindimva;Ndipo monga munthu wosalankhula, sinditsegula pakamwa panga.

14. Inde ndikunga munthu wosamva,Ndipo m'kamwa mwanga mulibe makani.

15. Pakuti ndikuyembekezani Inu, Yehova;Inu mudzayankha, Ambuye Mulungu wanga.

16. Pakuti ndinati, Asakondwerere ine:Pakuterereka phazi langa, asadzikuze pa ine.

17. Ndafikana potsimphina;Ndipo cisoni canga ciri pamaso panga cikhalire.

18. Pakuti ndidzafotokozera mphulupulu yanga;Nditenga nkhawa cifukwa ca chimo langa.

19. Koma adani anga ali ndi moyo, nakhalandi mphamvu:Ndipo akundida kopanda cifukwa acuruka.

20. Ndipo iwo akubwezera coipa pa cabwinoAtsutsana nane, popeza nditsata cabwino.

21. Musanditaye, Yehova:Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.

22. Fulumirani kundithandiza,Ambuye, cipulumutso canga.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 38