9. Pakuti ocita zoipa adzadulidwa:Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
10. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti:Inde, udzayang'anira mbuto yace, nudzapeza palibe.
11. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;Nadzakondwera nao mtendere wocuruka.
12. Woipa apangira ciwembu wolungama,Namkukutira mano.
13. Ambuye adzamseka:Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.
14. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;Alikhe ozunzika ndi aumphawi,Aphe amene ali oongoka m'njira:
15. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe,Ndipo mauta ao adzatyoledwa.
16. Zocepa zace za wolungama zikomaKoposa kucuruka kwao kwa oipa ambiri.
17. Pakuti manja a oipa adzatyoledwa:Koma Yehova acirikiza olungama.
18. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro:Ndipo cosiyira cao cidzakhala cosatha.
19. Sadzacita manyazi m'nyengo yoipa:Ndipo m'masiku a njala adzakhuta.
20. Pakuti oipa adzatayika,Ndipo adani ace a Yehova adzanga mafuta a ana a nkhosa:Adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
21. Woipa akongola, wosabweza:Koma wolungama acitira cifundo, napereka.
22. Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;Koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.
23. Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;Ndipo akondwera nayo njira yace.
24. Angakhale akagwa, satayikiratu:Pakuti Yehova agwira dzanja lace.