Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 37:23-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;Ndipo akondwera nayo njira yace.

24. Angakhale akagwa, satayikiratu:Pakuti Yehova agwira dzanja lace.

25. Ndinali mwana ndipo ndakalamba:Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.

26. Tsiku lonse acitira cifundo, nakongoletsa;Ndipo mbumba zace zidalitsidwa.

27. Siyana naco coipa, nucite cokoma,Nukhale nthawi zonse.

28. Pakuti Yehova akonda ciweruzo,Ndipo sataya okondedwa ace:Asungika kosatha:Koma adzadula mbumba za oipa.

29. Olungama adzalandira dziko lapansi,Nadzakhala momwemo kosatha.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 37