1. Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa,Usacite nsanje cifukwa ca ocita cosalungama.
2. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,Ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
3. Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma;Khala m'dziko, ndipo tsata coonadi.
4. Udzikondweretsenso mwa Yehova;Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
5. Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.
6. Ndipo adzaonetsa cilungamo cako monga kuunika,Ndi kuweruza kwako monga usana.
7. Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye:Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace,Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.
8. Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo:Usabvutike mtima ungacite coipa,
9. Pakuti ocita zoipa adzadulidwa:Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
10. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti:Inde, udzayang'anira mbuto yace, nudzapeza palibe.
11. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;Nadzakondwera nao mtendere wocuruka.
12. Woipa apangira ciwembu wolungama,Namkukutira mano.
13. Ambuye adzamseka:Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.