Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 35:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Njira yao ikhale ya mdima ndi yoterera,Ndipo mngelo wa Yehova awalondole.

7. Pakuti anandichera ukonde wao m'mbunamo kopanda cifukwa,Anakumbira moyo wanga dzenje kopanda cifukwa.

8. Cimgwere modzidzimutsa cionongeko;Ndipo ukonde wace umene anaucha umkole yekha mwini:Agwemo, naonongeke m'mwemo.

9. Ndipo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova:Udzasekera mwa cipulumutso cace.

10. Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani,Wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu,Ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?

11. Mboni za ciwawa ziuka,Zindifunsa zosadziwa ine.

12. Andibwezera coipa m'malo mwa cokoma,Inde, asaukitsa moyo wanga.

13. Koma ine, pakudwala iwowa, cobvala canga ndi ciguduli:Ndinazunza moyo wanga ndi kusala;Ndipo pemphero langa linabwera ku cifuwa canga.

14. Ndakhala ine monga ngad iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga:Polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wace.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 35