Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 35:11-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Mboni za ciwawa ziuka,Zindifunsa zosadziwa ine.

12. Andibwezera coipa m'malo mwa cokoma,Inde, asaukitsa moyo wanga.

13. Koma ine, pakudwala iwowa, cobvala canga ndi ciguduli:Ndinazunza moyo wanga ndi kusala;Ndipo pemphero langa linabwera ku cifuwa canga.

14. Ndakhala ine monga ngad iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga:Polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wace.

15. Ndipo pakutsimphina ine anakondwera, nasonkhana pamodzi:Akundipanda anandisonkhanira; ndipo sindinacidziwa:Ananding'amba osaleka:

16. Pakati pa onyodola pamadyerero,Anandikukutira mano.

17. Ambuye, mudzapenyerabe nthawi yanji?Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao,Wanga wa wokha kwa misona ya mkango.

18. Ndidzakuyamikanimumsonkhano waukuru:M'cikhamu ca anthu ndidzakulemekezani.

19. Adani anga asandikondwerere ine monyenga;Okwiya nane kopanda cifukwa asanditsinzinire.

20. Pakuti salankhula zamtendere:Koma apangira ciwembu odekha m'dziko.

21. Ndipo andiyasamira m'kamwa mwao;Nati, Hede, Hede, diso lathu lidacipenya.

22. Yehova, mudacipenya; musakhale cete:Ambuye, musakhale kutali ndi ine.

23. Galamukani, ndipo khalani maso kundiweruzira mlandu wanga,Mulungu wanga ndi Ambuye wanga,

24. Mundiweruze monga mwa cilungamo canu, Yehova Mulungu wanga;Ndipo asandisekerere ine.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 35