Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 34:6-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Munthu uyu wozunzika anapfuula, ndipo Yehova anamumva,Nampulumutsa m'masautso ace onse.

7. Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye,Nawalanditsa iwo.

8. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9. Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10. Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11. Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12. Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?

13. Uletse lilime lako lisachule zoipa,Ndipo milomo yako isalankhule cinyengo.

14. Pfutuka pazoipa, nucite zabwino,Funa mtendere ndi kuulondola.

15. Maso a Yehova ali pa olungama mtima,Ndipo makutu ace achereza kulira kwao.

16. Nkhopeya Yehovaitsutsananao akucita zoipa,Kudula cikumbukilo cao pa dziko lapansi.

17. Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva,Nawalanditsa ku masautso ao onse.

18. Yehova ali pafupi ndi iwo a mtimawosweka,Apulumutsa iwo a mzimu wolapadi,

Werengani mutu wathunthu Masalmo 34