Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 34:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndidzalemekeza Yehova nyengo zonse;Kumlemekeza kwace kudzakhala m'kamwa mwanga kosalekeza.

2. Moyo wanga udzatamanda Yehova;Ofatsa adzakumva nadzakondwera.

3. Bukitsani pamodzi ndine ukuru wa Yehova,Ndipo tikweze dzina lace pamodzi.

4. Ndinafuna Yehova ndipo anandibvomera,Nandlianditsa m'mantha anga Onse.

5. Iwo anayang'ana Iye nasanguruka;Ndipo pankhope pao sipadzacita manyazi,

6. Munthu uyu wozunzika anapfuula, ndipo Yehova anamumva,Nampulumutsa m'masautso ace onse.

7. Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye,Nawalanditsa iwo.

8. Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino;Wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

9. Opani Yehova, inu oyera mtima ace;Cifukwa iwo akumuopa Iye sasowa.

10. Misona ya mkango isowa nimva njala:Koma iwo akufuna Yehova sadzasowa kanthu kabwino.

11. Idzani ananu ndimvereni ine:Ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

12. Munthu wokhumba moyo ndani,Wokonda masiku, kuti aone zabwino?

Werengani mutu wathunthu Masalmo 34