Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 32:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wodala munthuyo wokhululukidwa chimo lace;Wokwiriridwa coipa cace.

2. Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zace;Ndimo mumzimu mwace mulibe cinyengo.

3. Pamene ndinakhala cete mafupa anga anakalambaNdi kubuula kwanga tsiku lonse.

4. Cifukwa usana ndi usiku dzanja lanu linandilemera ine;Uwisi wanga unasandulika kuuma kwa malimwe.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 32