Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 29:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,Perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2. Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lace:Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

3. Liu la Yehova liri pamadzi;Mulungu wa ulemerero agunda,Ndiye Yehova pa madzi ambiri.

4. Liu la Yehova ndi lamphamvu;Liu la Yehova ndi lalikurukuru.

5. Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;Inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebano.

6. Aitumphitsa monga mwana wa ng'ombe;Lebano ndi Sirio monga msona wa njati.

7. Liu la Yehova ligawa malawi a moto.

8. Liu la Yehova ligwedeza cipululu;Yehova agwedeza cipululu ca Kadese.

9. Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,Ndipo lipulula nkhalango:Ndipo m'Kacisi mwace zonse ziri m'mwemo zimati, Ulemerero:

10. Yehova anakhala pa Cigumula:Inde Yehova akhala mfumu ku nthawi yomka muyaya.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 29