Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 22:22-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga:Pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.

23. Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;Inu nonse mbumba ya Yakobo, mumcitire ulemu;Ndipo mucite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israyeli.

24. Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika;Ndipo sanambisira nkhope yace;Koma pompfuulira Iye, anamva.

25. Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukuru:Zowinda zanga ndidzazicita pamaso pa iwo akumuopa Iye.

26. Ozunzika adzadya nadzakhuta:Adzayamika Yehova iwo amene amfuna:Ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.

27. Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukila nadzatembenukira kwa Yehova:Ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.

28. Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;Iye acita ufumu mwa amitundu.

29. Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira:Onse akutsikira kupfumbi adzawerama pamaso pace,Ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wace.

30. Mbumba ya anthu idzamtumikira;Kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.

31. Iwo adzadza nadzafotokozera cilungamo caceKwa anthu akadzabadwa, kuti Iye anacicita.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 22