21. Ndipulumutseni m'kamwa mwa mkango;Inde mwandiyankha ine ndiri pa nyanga za njati,
22. Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga:Pakati pa msonkhano ndidzakulemekezani.
23. Inu akuopa Yehova, mumlemekeze;Inu nonse mbumba ya Yakobo, mumcitire ulemu;Ndipo mucite mantha ndi Iye, inu nonse mbumba ya Israyeli.
24. Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika;Ndipo sanambisira nkhope yace;Koma pompfuulira Iye, anamva.
25. Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukuru:Zowinda zanga ndidzazicita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
26. Ozunzika adzadya nadzakhuta:Adzayamika Yehova iwo amene amfuna:Ukhale moyo mtima wako nthawi zonse.
27. Malekezero onse a dziko lapansi adzakumbukila nadzatembenukira kwa Yehova:Ndipo mafuko onse a amitundu adzagwadira pamaso panu.
28. Pakuti ufumuwo ngwa Yehova;Iye acita ufumu mwa amitundu.
29. Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira:Onse akutsikira kupfumbi adzawerama pamaso pace,Ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wace.
30. Mbumba ya anthu idzamtumikira;Kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.