Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 20:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Likutumizire thandizo loturuka m'malo oyera,Ndipo likugwirizize kucokera m'Ziyoni;

3. Likumbukile zopereka zako zonse,Lilandire nsembe yako yopsereza;

4. Likupatse ca mtima wako,Ndipo likwaniritse upo wako wonse.

5. Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu,Ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera:Yehova akwaniritse mapempho ako onse.

6. Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wace;Adzambvomereza m'Mwamba mwace moyeraNdi mphamvu ya cipulumutso ca dzanja lace lamanja.

7. Ena atama magareca, ndi ena akavalo:Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.

8. Iwowa anagonieka, nagwa:Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 20