Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 18:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,Nafukuka maziko a dziko lapansi,Mwa kudzudzula kwanu, Yehova,Mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.

16. Anatuma kucokera m'mwamba, ananditenga;Anandibvuula m'madzi ambiri.

17. Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,Ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18. Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga.

19. Ananditurutsanso andifikitse motakasuka;Anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20. Yehova anandibwezera monga mwa cilungamo canga;Anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21. Pakuti ndasunga njira za Yehova,Ndipo sindinacitira coipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22. Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga,Ndipo malemba ace sindinawacotsa kwa ine.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 18