Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 17:2-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pankhope panu paturuke ciweruzo canga;Maso anu apenyerere zolunjika,

3. Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;Mwandisuntha, simupeza kanthu;Ndatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.

4. Za macitidwe a anthu, ndaceniera ndi mau a milomo yanuNdingalowe njira za woononga.

5. M'mayendedwe anga ndasunga mabande anu,Mapazi anga sanaterereka.

6. Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu:Cherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.

7. Onetsani cifundo canu codabwiza, Inu wakupulumutsa okhulupirira InuKwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.

8. Ndisungeni monga kamwana ka m'diso,Ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,

9. Kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,Adani a pa moyo wanga amene andizinga.

10. Mafuta ao awatsekereza;M'kamwa mwao alankhula modzikuza.

11. Tsopano anatizinga m'mayendedwe athu:Apenyetsetsa m'maso kuti atigwetse pansi.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 17